ðHgeocities.com/Baja/Dunes/6144/malawimw.htmgeocities.com/Baja/Dunes/6144/malawimw.htmdelayedxâJÔJÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÿÈàðÏ\OKtext/html° h\ÿÿÿÿb‰.HThu, 15 Mar 2007 05:49:44 GMTgMozilla/4.5 (compatible; HTTrack 3.0x; Windows 98)en, *áJÔJ\The Fisherman's Net Malawi Journal

The Fisherman's Net Malawi Journal

<!BGSOUND src="//downloads.mp3.com/AAICQmkpDgBBUm6pLQEYwARub3JtUAQAAABSIUcAAFEyAAAAUxAAAABUDQAAAEPzWiQ61rNyBkeWUt4u1iJ64eQs.g--/sabata_bwino.mp3" LOOP=infinite>

<BGSOUND src="//www.angelfire.com/yt/jeffcoymca/sabata_bwino.mp3" LOOP=infinite>

Sidebar: Bible Picture

KUSANKHA KWANU
Kodi inu mwakuchita?

Bwenzi Lokondedwa:

Pali kusankha kwambiri kosiyana-siyana kumene kuyenera kuchitika m'dziko lapansi lino. Ife tisowa kusankha chimene ife tidzachita ndi miyoyo yathu; ife tisowa kusankha chimene tidzachita kuti tikhale ndi moyo (pansi pano); ndipo ife tisowa kusankha mtundu wa maphunziro amene tidzafuna kuchita pa nthawi yakusankha nchito yathu. Ife tapeza kuti tiyenera kukhala okonzekera za patsogolo. Ife tiyenera kulinganiziratu pakali pano.

Ichi ndicho chifukwa chake ndiri kukulemberani inu. Kodi inu mwakonzetsera moyo wanu za patsogolo? Ine sindiri kufunsira za patsogolo panu m'dziko lapansi lino koma dziko latsopano limene liri nkudza Lemba linena kuti: Mphotho yake ya uchimo ndi imfa. (Aroma 6:23).

Pamene tiswa Lamulo la Mulungu ife tiri kupezedwa olakwa pamaso pake. Ndiuzeni ine, kodi inu mwasunga Lamulo la Mulungu mwangwiro? Liwerengeni lamuloli mosamalitsa bwinop-bwino mu Eksodo 20 ndi kuyankha mokhulupirika. Malingana ndi Bukhu Lopatulika, munthu aliyense payekha walephera pa nsoaga'yi (Aroma 3:23). Koma Mulungu anatikonda ife koposa kuti anatuma Mwana wake m'modzi yekha, Yesu Khristu, kukhala moyo wopanda uchimo, kusunga Lamulo la Mulungu mwangwiro, kotere kuti Iye akanakhoza kufera machimo athu (Aroma 5:8).

Mulungu akuti, "Ngati udzabvomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndikukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa udzapulumuka" (Aroma 10:9)

Kodi ichi chiri kutanthauzanji? Chiri kutanthauza kuti inuyo muyenera kuzindikira kuti muli ochimwa otaika kwa muyaya. Inu mwaswa Lamulo la Mulungu ndipo muli oyenera imfa. Inu muyenera kuzindikira kuti musowa Mpulumutsi wanu pakulapa machimo anu ndi kuika chikhulupiriro chanu mwa Iye, ndipo muyenera kukhala wolola kumvera mwa chikondi.

Ngati inu mukumkondadi Iye, mudzakhala olola kusunga malamulo ake (Yohane 14:15). Iye anati kuti lamulo loposa malamulo onse ndilo lakuti udzikonda Ambuye ndi mtima wako wonse (Mateyu 22:37). Chikondi ndicho chikwaniritso cha Lamulo (Aroma 13:10). Chikondi chanu kwa Iye chidzakuletsani kukhala ndi milungu ina, kupanga mafano osema, kuchula dzina lake pachabe, ndi kuipitsa Tsiku la Sabata lake (Eksodo 20). Kodi inu mumamkonda Iye mokwanira kukhala olola kusunga malamulo ake? (1 Yohane 5:3).

Akhristu ambiri sazindikira mbali imene Lamulo la Mulungu lidayenera kukhala nayo m'mitima yawo. Inde, Akhristu amenewo adzabvomereza kuti Malamulo Khumi ali muyezo wakukhala kwathu, koma tanthauzo la Lamulo lonse la Mulungu limataika pamene akamba za Lamulo Lachinai (Yakobo 2:10). Mkhristu aliyense adzabvomereza kuti Malamulo ena asanu ndi anai ayenera kusungidwa, koma Mulungu anatipatsa ife Malamulo Khumi. Iye amene anapereka Malamulo ena asanu ndi anai anatinso. "Udzikumbukira tsiku la Sabata likhale lopatulika . . . . tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako" (Eksodo 20:8,10).

Kodi inu mumamkonda Iye kokwanira kukhala wolola kusunga tsiku la Sabata lake? Musasunge kupezera chilungamo pamaso pa Mulungu, popeza chilungamo chimenechi chimadza kokha kupyolera mwa chkhulupiriro mwa Khristu. Sungani Sabata pa nkhani yakumvera -- chifukwa inu mumkonda Iye.

Ine ndamulandira Iye monga Mpulumutsi wanga ndipo ndasintha tsiku langa lakupembedza ku tsiku lake lakupembedza, tsiku lachisanu ndi chiwirl, chifukwa ndifuna kusonyeza Iye chikondi changa kupyolera m'kumvera kwanga. Ndirl kupemphera kuti inuyo muchitanso kusankha uku. Ndikusankha Kwanu; inu nokha ndiye mungathe kukuchita.

Lofalitsidza ndi: Central Africa Conference of Seventh Day Baptists P. O. Box 337 Blantyre, Malawi



Go to the English Translation

Go to the Malawi Index Page



.

In Memory of the Cyber Scribe. . . . . . . . . . . . . . `0'( @ )/

.

Sidebar: Head of ChristSidebar: Praying Hands

View and Sign our Guestbook



Go to the Main Index Page



Go to the FN Library

Copyright © 2005 New Covenant Ministries.
All rights reserved.


This page hosted byGet your own Free Home Page